Wa Ganyu
Anthu adadzidzimuka usiku wa Lolemba m’sabatayi atamva mfuu wa zipolopolo pa bwalo la Bingu National mumzinda wa Lilongwe. Sadali mabuleti a zigoli koma machaka enieni omwe pamapeto adakhazika pansi mkulu wina amene akumuganizira kuti amafuna kuba.
Apolisi ya Lingadzi atsimikiza kuti kulirako kudalidi wa mpholopolo zomwe zidagwetsa Daniel Masautso ndikupinda mwendo wamanzere pomuganizira kuti amaba pa bwalo la zamasewero la Bingu.
Mneneri wa polisi ya Lingadzi, Maria Kumwenda wati apolisi adamva phokoso pa bwalolo ndipo ataponya maso patali adaona woganiziridwayo atanyamula thumba.
“Pa nthawiyo adaona Masautso atanyamula matumba awiri momwe mudali zokhalira za kuchimbudzi,” adatero mneneriyo.
Koma mkuluyo akuti adayamba kuthawa zomwe zidapangitsa apolisi kuti athira machaka woganiziridwayo ndipo adalunjika mwendo wa manzere. Kudali kovuta kuti Masautso aphuphe koma kuvala unyolo koma akumva kuwawa.
Kumwenda wati woganiziridwayo athamanga naye pachipatala cha gulupu ku Lilongwe komwe akulandira thandizo lachipatala.
Wapolisiyo wati akumufunira woganiziridwayo kuchita kwamsanga kuti akayankhe mlandu.
Bwalo la Bingu lakhala pa diwa wa anthu akuba amene nthawi zonse amapezeka akuba katundu wosiyanasiyana.





